Leviticus 18:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usagone ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa bambo wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, ngakhale abadwire kwanu kapena kuchilendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usamavula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Usagonane ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa abambo ako, kapena mwana wamkazi wa amayi ako, kaya anabadwira mʼnyumba mwanu kapena kwina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usamabvula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.