Leviticus 19:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akagona ndi mkazi amene ali mdzakazi wofunsidwa mbeta ndi munthu wina, koma wosaomboledwa kapenanso asanalandire ufulu wake, aimbidwe mlandu. Onsewo asaphedwe, chifukwa mkaziyo anali asanalandire ufulu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu agonana ndi kapolo wamkazi amene wafunsidwa mbeta ndi munthu wina, koma sanawomboledwe kapenanso kulandira ufulu wake, alangidwe. Koma onsewa asaphedwe, chifukwa mkaziyo anali asanalandire ufulu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo.