Leviticus 19:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe achite mwambo wopepesera machimo a munthuyo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopepesera kupalamulayo pamaso pa Chauta, chifukwa cha tchimo limene munthuyo adachita, ndipo tchimo adachitalo lidzakhululukidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe achite chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula pamaso pa Yehova, chifukwa cha kuchimwa adachimwaku; ndipo adzakhululukidwa chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwaku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo wansembe achite nayo mwambo wopepesera chifukwa cha kupalamula kumene anachita pamaso pa Yehova. Akatero tchimo lake lidzakhululukidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe acite comtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yoparamula pamaso pa Yehova, cifukwa ca kucimwa adacimwaku; ndipo adzakhululukidwa cifukwa ca kucimwa kwace adacimwaku.