Leviticus 19:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamene muloŵa m'dzikomo ndi kubzala mitengo yamitundumitundu ya zipatso, zipatsozo zikhale zoletsedwa. Zikhale zoletsedwa kwa inu zaka zitatu, musadye pa nthaŵi imeneyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzala mitengo ya mitundumitundu ikhale ya chakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mukadzalowa mʼdzikomo ndi kudzala mtengo wa mtundu uliwonse wa zipatso, zipatso zakezo mudzaziyese ngati zodetsedwa. Ndiye kuti kwa zaka zitatu zidzakhale zoletsedwa kwa inu. Musadzazidye nthawi imeneyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzalamitengo yamitundumitundu ikhale ya cakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa.