Leviticus 19:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Musamapita kwa anthu olankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa anyanga. Musaŵafunefune kuti angakuipitseni. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Musamapite kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa owombeza. Musamawafunefune kuti angakuyipitseni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.