Leviticus 2:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chopereka cha chakudya chimene upereka kwa Chauta chikhale chopanda chofufumitsira, pakuti suyenera kupereka kwa Chauta nsembe yotentha pa moto, imene ili ndi chofufumitsira kapena uchi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nsembe iliyonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi chotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yachotupitsa, kapena yauchi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Nsembe ya chakudya chilichonse imene ubweretsa kwa Yehova ikhale yopanda yisiti, pakuti suyenera kupereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto imene ili ndi yisiti kapena uchi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nsembe iri yonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi cotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yacotupitsa, kapena yauci.