Leviticus 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ziŵirizo ungathe kubwera nazo ngati nsembe ya zokolola zoyambirira zopereka kwa Chauta. Koma usazitenthere pa guwa kuti zipereke fungo lonunkhira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize pa guwa la nsembe zichite fungo lokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga copereka ca zipatso zoyamba muzipereka izi: koma asazifukize pa guwa la nsembe zicite pfungo lokoma.