Leviticus 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ukamapereka kwa Chauta chopereka cha chakudya choyamba kucha, nsembeyo ikhale ya mbeu zatsopano zokazinga ndi zopunthapuntha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ukabwera nayo nsembe yaufa ya zipatso zoyamba kwa Yehova, uzibwera nayo nsembe yako ya zipatso zoyamba ikhale ya ngala zoyamba kucha, zoumika pamoto, zokonola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mukamapereka kwa Yehova chopereka cha chakudya choyamba kucha, choperekacho chikhale cha chipatso chatsopano chokazinga pa moto ndi chopunthapuntha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ukabwera nayo nsembe yaufa ya zipatso zoyamba kwa Yehova, uzibwera nayo nsembe yako ya zipatso zoyamba ikhale ya ngala zoyamba kuca, zoumika pamoto, zokonola.