Leviticus 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe atenthe chigawo cha mbeu zopunthapuntha zija ndi cha mafuta, ndiponso lubani wake yense, kuti ikhale nsembe yachikumbutso. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono wansembe atenthe gawo la chopereka chopunthapuntha chija kuti chikhala ufa wachikumbutso ndi cha mafuta pamodzi ndi lubani yense kuti Yehova alandire mʼmalo mwa zopereka zonse. Ichi ndi chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe atenthe cikumbutso cace, atatapa pa tirigu wace wokonola, ndi pa mafuta ace, ndi kutenga libano lace lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.