Leviticus 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zotsala za chopereka cha chakudyacho zikhale za Aroni pamodzi ndi ana ake. Chimenecho ndicho chigawo chopatulika kopambana, chifukwa chatapidwa pa nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zotsala za nsembe ya chakudyazo ndi za Aaroni pamodzi ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cotsalira ca nsembe yaufa cikhale ca Aroni ndi ana ace; ndico copatulikitsa ca nsembe zamoto za Yehova.