Leviticus 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ubwere nacho chopereka chimenechi kwa Chauta, ndipo utachipereka kwa wansembe, iyeyo abwere nacho ku guwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera nacho kwa wansembe, iyeyo apite nacho ku guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu azibwera ndi nsembe za chakudya zimene wapanga ndi zinthu zimenezi. Atachipereka kwa wansembe, iyeyu adzipita nacho ku guwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera naco kwa wansembe, iyeyo apite naco ku guwa la nsembe.