Leviticus 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo wansembeyo atengeko gawo lina la choperekacho kusonyeza kuti chaperekedwa kwa Chauta, tsono achitenthe paguwapo. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe pa guwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembeyo atengeko gawo lina la nsembeyo kukhala ufa wachikumbutso kuti ilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse ndipo ayitenthe pa moto monga nsembe yopsereza ya fungo lokomera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembeyo atengeko cikumbutso pa nsembe yaufa, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndico nsembe yamoto ya pfungo lokoma la kwa Yehova.