Leviticus 20:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akakwatira mkazi, nakwatiranso mai wake wa mkaziyo, kuteroko nkuchita chinthu choipa kwambiri. Onsewo ayenera kuŵatentha pa moto, mwamunayo pamodzi ndi akazi omwewo, kuti chinthu choipa kwambiri chotere chisapezeke pakati panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wake chochititsa manyazi ichi; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale chochititsa manyazicho pakati pa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu akwatira mkazi, nakwatiranso amayi ake, chimenecho ndi chinthu choyipa kwambiri. Mwamunayo pamodzi ndi akaziwo ayenera kutenthedwa pa moto kuti chinthu choyipa chotere chisapezekenso pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wace cocititsa manyazi ici; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale cocititsa manyazico pakati pa inu.