Leviticus 20:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, onse aŵiriwo achita chinthu chochititsa manyazi, ndipo onsewo aphedwe pakhamu pa anthu a mtundu wao. Chifukwa aphwanya malamulo motero, alipire choipa chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake, kapena mwana wamkazi wa amayi ake, ndipo iwo nʼkugonana, ndiye kuti achita chinthu chochititsa manyazi. Onse awiri ayenera kuchotsedwa pa gulu la abale awo. Tsono popeza munthuyo wachititsa manyazi mlongo wake, adzayenera kulandira chilango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akatenga mlongo wace, mwana wamkazi wa atate wace, kapena mwana wamkazi wa mai wace, nakaona thupi lace, ndi mlongoyo akaona thupi lace; cocititsa manyazi ici; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anabvula mlongo wace; asenze mphulupulu yace.