Leviticus 20:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akagona ndi mkazi wosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, nayenso mkaziyo wadzivula. Onse aŵiriwo achotsedwe pakati pa anthu anzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakamvula, anavula kasupe wake, ndi iye mwini anavula kasupe wa nthenda yake; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi pa nthawi yake yosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, ndipo mkaziyo wadzivulanso. Onse awiri achotsedwe pakati pa anthu anzawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakambvula, anabvula kasupe wace, ndi iye mwini anabvula kasupe wa nthenda yace; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao.