Leviticus 20:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uza Aisraele kuti: Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala nao m'dziko mwanu, akapereka ana ake kwa Moleki, aphedwe: anthu am'dzikomo amponye miyala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unenenso kwa ana a Israele ndi kuti, Aliyense wa ana a Israele, kapena wa alendo akukhala m'Israele, amene apereka mbeu zake kwa Moleki, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Unenenso kwa ana a Israyeli ndi kuti, Ali yense wa ana a Israyeli, kapena wa alendo akukhala m'Israyeli, amene apereka mbeu zace kwa Moleke, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala.