Leviticus 20:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musatsanzire miyambo ya mtundu wa anthu amene ndikuupirikitsa inu mukufika. Iwo ankachita zimenezi, nchifukwa chake ndidanyansidwa nawo kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musatsanzire miyambo ya mitundu ya anthu imene ndi kuyipirikitsa inu mukufika. Chifukwa iwo anachita zinthu zonsezi, ndipo Ine ndinanyansidwa nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamatsata miyambo ya mtundu umene neliucotsa pamaso panu; popeza anacita izi zonse, nelinalema nao.