Leviticus 20:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inuyo ndakuuzani kuti: Mudzalandira dziko lao, ndipo ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale lanu, dziko lake lamwanaalirenji. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ine ndinakuwuzani kuti, ‘Mudzatenga dziko lawo. Ine ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale cholowa chanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu yina ya anthu.