Leviticus 20:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoipitsidwa ndi zosaipitsidwa, pakati pa mbalame zosaipitsidwa ndi zoipitsidwa. Musadziipitse pakudya nyama kapena mbalame, kapenanso zinthu zilizonse zimene zadzaza pansi pano, zomwe ndazipatula kuti inu muzidziŵe kuti nzoipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kalikonse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Chifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoyeretsedwa ndi nyama zodetsedwa ndiponso pakati pa mbalame zoyeretsedwa ndi mbalame zodetsedwa. Musadzidetse pakudya nyama iliyonse kapena mbalame, kapena chilichonse chimene chimakwawa pansi, chimene Ine ndachipatula kuti chikhale chodetsedwa kwa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kali konse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.