Leviticus 20:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu ameneyo ndidzamfulatira, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake, chifukwa wapereka ana ake kwa Moleki ndi kuipitsa malo anga oyera, ndiponso waipitsa dzina langa loyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu ameneyo ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anzake.’ Popereka mwana wake kwa Moleki, wadetsa malo anga wopatulika ndi kuyipitsa dzina langa loyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumcotsa pakati pa anthu a mtundu wace; popeza anapereka a mbeu zace kwa Moleke, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.