Leviticus 20:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ineyo ndidzamfulatira munthu ameneyo ndi banja lake lonse. Ndidzaŵachotsa pakati pa anthu anzao, pamodzi ndi onse amene amaŵatsanzira nadziipitsa pakupembedza Moleki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ineyo ndidzamufulatira pamodzi ndi banja lake. Ndidzawachotsa pakati pa anthu anzawo onse amene anamutsatira, nadziyipitsa okha popembedza Moleki.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lace, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi cigololo kukacita cigololo kwa Moleke, kuwacotsa pakati pa anthu a mtundu wao.