Leviticus 21:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu amene ali mkulu wa ansembe onse, amene adamdzoza pa mutu ndi mafuta, ndiponso amene adapatulidwa pakumuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake, kapena kung'amba zovala zake kusonyeza kuti ali pamaliro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ake, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pake, amene anamdzaza dzanja kuti avale zovalazo, asawinde, kapena kung'amba zovala zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Munthu amene ali mkulu wa ansembe pakati pa abale ake, amene anamudzoza pomutsanulira mafuta pamutu pake, ndiponso amene anapatulidwa pomuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake kapena kungʼamba zovala zake kusonyeza kuti ali pa chisoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ace, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pace, amene anamdzaza dzanja kuti abvale zobvalazo, asawinde, kapena kung'amba zobvala zace.