Leviticus 21:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
asakwatire mkazi wamasiye kapena mkazi wosudzulidwa, kapenanso mkazi wachiwerewere. Koma akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, amene sanadziŵeko mwamuna,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wachigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wake akhale mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asakwatire mkazi wamasiye, mkazi wosudzulidwa, kapena mkazi wachiwerewere, koma akwatire namwali wosadziwa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wacigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wace akhale mkazi wace.