Leviticus 21:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma asadzabwere pafupi ndi nsalu yochinga, kapena kuyandikira guwa, chifukwa ali ndi chilema, kuwopa kuti angadzaipitse malo anga oyera. Pakuti Ine ndine Chauta amene ndidapatula malo amenewo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma asafike ku nsalu yotchinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali nacho chilema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chifukwa cha kulumala kwake, sayenera kuyandikira katani kapena kufika pa guwa kuti angadetse malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma asafike ku nsaru yocinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali naco cirema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.