Leviticus 21:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amakhala pafupi naye, poti chikhalire alibe mwamuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi chifukwa cha mlongo wake weniweni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse chifukwa cha iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amadalira iye chifukwa sanakwatiwe. Iye akhoza kudzidetsa pokhudza thupi lakufa la mchemwali wake wosakwatiwa yekha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi cifukwa ca mlongo wace weni weni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse cifukwa ca iwowa.