Leviticus 22:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wansembe akagula kapolo ndi ndalama kuti akhale wake, kapoloyo angathe kudya nao zinthuzo. Ndipo onse amene abadwa m'nyumba mwa wansembe angathe kudyako chakudya chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wansembe atakagula munthu ndi ndalama zake, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yake, adyeko mkate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kapolo amene wagulidwa ndi ndalama kapena kubadwira mʼbanja la wansembe angathe kudya chakudya cha wansembeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wansembe atakagula munthu ndi ndarama zace, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yace, adyeko mkate wace.