Leviticus 22:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mwana wamkazi wa wansembeyo akakhala wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, nabwerera ku nyumba ya bambo wake monga pa nthaŵi ya utsikana wake, angathe kudyako chakudya cha bambo wake. Koma wapadera asadyeko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wochotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera kunyumba ya atate wake, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wake; koma mlendo asamadyako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mwana wamkazi wa wansembe amene ali wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, komanso anabwerera ku nyumba ya abambo ake monga pa nthawi ya utsikana wake, angathe kudya chakudya cha abambo ake. Mlendo asadye chakudya chopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wocotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera ku nyumba ya atate wace, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wace; koma mlendo asamadyako.