Leviticus 22:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wapadera akadyako chinthu chopatulika mosadziŵa, alipire wansembe chifukwa cha chinthucho, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu akadyako chinthu chopatulika mosadziwa, azionjezapo limodzi la magawo asanu, nalipereke kwa wansembe, pamodzi ndi chopatulikacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu wina aliyense adya chopereka chopatulika mosadziwa, munthuyo amubwezere wansembe chinthu chopatulikacho ndipo awonjezerepo limodzi la magawo asanu a chinthucho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu akadyako cinthu copatulika mosadziwa, azionjezapo limodzi la magawo asanu, nalipereke kwa wansembe, pamodzi ndi copatulikaco.