Leviticus 22:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraelewo pakuŵalola kudya zakudya zao zopatulika. Inetu ndine Chauta, amene ndimazipatula.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraeli powalola kudya zakudya zawo zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndimawayeretsa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwaparamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.