Leviticus 22:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uza Aroni, ana ake ndi Aisraele onse kuti, mwina munthu wa m'banja la Aisraele, kapena mlendo wokhala m'dziko la Israele, adzabwera ndi chopereka chake kuti aperekere chimene wachilumbirira. Mwina adzabwera ndi chopereka kuti chikhale nsembe yaufulu yopereka kwa Chauta ngati nsembe yopsereza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana onse a Israele, nuti nao, Aliyense wa mbumba ya Israele, kapena wa alendo ali m'Israele, akabwera nacho chopereka chake, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yankhula ndi Aaroni, ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse, ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati wina aliyense wa inu, Mwisraeli kapena mlendo amene akukhala mu Israeli abwera ndi mphatso ya nsembe yopsereza kwa Yehova, kupereka chimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nena ndi Aroni, ndi ana ace amuna, ndi ana onse a Israyeli, nuti nao, Ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena wa alendo ali m'Israyeli, akabwera naco copereka cace, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;