Leviticus 22:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uza Aroni pamodzi ndi ana ake aamuna kuti azilemekeza zinthu zopatulika zimene Aisraele amapereka kwa Ine, kuti angaipitse dzina langa loyera. Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nena ndi Aroni ndi ana ake amuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uza Aaroni ndi ana ake kuti azilemekeza zinthu zopatulika zimene Aisraeli azipereka kwa Ine, kuti asayipitse dzina langa loyera. Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nena ndi Aroni ndi ana ace amuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israyeli, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.