Leviticus 22:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina munthu wina adzapereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, kuti achitedi zimene adalumbirira, kapena kuti ikhale nsembe yaufulu. Ngati ndi ng'ombe kapena nkhosa, kuti Chauta ailandire, iyenera kukhala yopanda chilema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa chowinda chachikulu, kapena ya pa chopereka chaufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda chilema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene wina aliyense abweretsa ngʼombe kapena nkhosa kuti ikhale nsembe yachiyanjano kwa Yehova, kukwaniritsa zimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, nyamayo iyenera kukhala yangwiro ndi yopanda chilema kuti ilandiridwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa cowinda cacikuru, kapena ya pa copereka caufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda cirema.