Leviticus 22:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mungathe kupereka ng'ombe yamphongo kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi, kuti ikhale nsembe yaufulu, koma ikakhala nsembe yolumbirira, singathe kulandiridwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mungathe kupereka ngʼombe yayimuna kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi kukhala nsembe yaufulu. Koma simungayipereke ngati nsembe yoperekera zimene munalumbirira chifukwa sidzalandiridwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yocepa ciwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa cowinda siidzalandirika.