Leviticus 22:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo musapereke nyama iliyonse ya mtundu umenewo imene mwailandira kwa mlendo, kuti ikhale nsembe ya chakudya chopereka kwa Chauta. Zimenezi sadzazilandira chifukwa zili ndi chilema ndipo nzopunduka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale chakudya cha Mulungu wanu; popeza zili nako kuvunda kwao; zili ndi chilema; sizidzalandirikira inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo musalandire nyama zotere kuchokera kwa mlendo ndi kuzipereka kukhala zakudya za Mulungu wanu. Zimenezi sizidzalandiridwa mʼmalo mwanu chifukwa zili ndi chilema ndipo ndi zolumala.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale cakudya ca Mulungu wanu; popeza ziri nako kubvunda kwao; ziri ndi cirema; sizidzalandirikira inu.