Leviticus 22:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ng'ombe, nkhosa kapena mbuzi ikabadwa, ikhale ndi make masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo kuyambira pa tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka m'tsogolo mwake, ingathe kulandiridwa kuti ikhale nsembe yopsereza, yopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi make masiku asanu ndi awiri; kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo mwake, idzalandirika ngati chopereka nsembe yamoto ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene mwana wangʼombe, mwana wankhosa kapena mwana wambuzi wabadwa, akhale ndi make kwa masiku asanu ndi awiri. Kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka mʼtsogolo mwake, angathe kulandiridwa kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuyambira tsiku lacisanu ndi citatu ndi m'tsogolo mwace, idzalandirika ngati copereka nsembe yamoto ya Yehova.