Leviticus 22:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wina aliyense mwa zidzukulu zake pa mibadwo yonse, akayandikira zopatulika zimene Aisraele adazipereka kwa Chauta, pamene iyeyo ali woipitsidwa, asaonekenso pamaso panga. Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uwawuze kuti ngati wina aliyense mwa zidzukulu zawo mʼmibado yonse imene ikubwera adzayandikira zinthu zopatulika zimene ana a Israeli apereka kwa Yehova, ali wodetsedwa, ameneyo achotsedwe pamaso pa Yehova. Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nena nao, Ali yense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israyeli azipatulira Yehova, pokhala ali naco comdetsa cace, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.