Leviticus 22:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense mwa zidzukulu za Aroni amene ali ndi khate kapena amene amatulutsa zoipa m'thupi mwake, asadyeko zinthu zopatulika mpaka atayeretsedwa. Mwina wansembe angathe kukhudza chinthu choipitsidwa chifukwa chokhudzana ndi chinthu chakufa, kapena angathe kutaya mbeu yake yaumuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu aliyense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo aliyense wokhudza chinthu chodetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Munthu aliyense mwa zidzukulu za Aaroni amene ali ndi khate kapena amatulutsa zoyipa mʼthupi mwake, asadye zinthu zopatulika mpaka atayeretsedwa. Wansembe angakhale wodetsedwa atakhudzana ndi chinthu chimene chadetsedwa ndi chinthu chakufa kapena kukhudza munthu amene wataya umuna,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu ali yense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo ali yense wokhudza cinthu codetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;