Leviticus 22:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzakhala woyeretsedwa dzuŵa litaloŵa, ndipo pambuyo pake adzatha kudyako zinthu zopatulikazo, poti zimenezo ndi chakudya chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo adzakhala woyeretsedwa pamene dzuwa lalowa, ndipo angathe kudya chopereka chopatulikacho popeza ndi chakudya chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pace adyeko zoyerazo, popeza ndizo cakudya cace.