Leviticus 23:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chopereka cha chakudya yopereka pamodzi ndi nkhosayo ikhale makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa yopereka pamodzi ndi nkhosayo, ikhale ya vinyo wokwanira ngati lita limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nsembe yaufa yake ikhale awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, ichite fungo lokoma; ndi nsembe yake yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chopereka chachakudya chake chikhale cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta kuti chikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa chake chikhale vinyo wa malita anayi ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nsembe yaufa yace ikhale awiri a magawo khumi a ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, icite pfungo lokoma; ndi nsembe yace yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.