Leviticus 23:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musadye buledi kapena tirigu wouma kapena wamuŵisi tsikuli lisanafike, mpaka mutabwera nayo nsembe kwa Mulungu wanu. Limeneli ndilo lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza nacho chopereka cha Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musadye buledi aliyense kapena tirigu wokazinga, kapena wamuwisi mpaka tsiku limene mwabwera ndi chopereka ichi kwa Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza naco copereka ca Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse.