Leviticus 23:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'nyumba mwanu mutenge buledi muŵiri wa ufa wokwanira makilogaramu aŵiri, kuti amuweyule. Akhale wa ufa wosalala, ndipo aphikidwe ndi chofufumitsira, kuti akhale mphatso yoyamba yopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutuluke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi chotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kulikonse kumene mukukhala, mubwere pamaso pa Yehova ndi buledi muwiri wa ufa wosalala wa makilogalamu awiri, ophikidwa ndi yisiti kuti akhale nsembe yoweyula ya zakudya zoyamba kucha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muturuke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi cotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.