Leviticus 23:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muperekenso tonde mmodzi ngati nsembe yopepesera machimo, ndi anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi ngati nsembe yachiyanjano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukonzenso mwanawambuzi mmodzi akhale nsembe yauchimo, ndi anaankhosa awiri a chaka chimodzi akhale nsembe yoyamika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mupereke mbuzi imodzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndiponso ana ankhosa awiri, aliyense wa chaka chimodzi kuti akhale nsembe yachiyanjano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukonzenso mwana wa mbuzi mmodzi akhale nsembe yaucimo, ndi ana a nkhosa awiri a caka cimodzi akhale nsembe yoyamika.