Leviticus 23:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uza Aisraele kuti, ‘Masiku achikondwerero osankhidwa olemekeza Chauta, amene mudzaŵalengeza kuti akhale masiku oyera amisonkhano, masiku achikondwerero amene Ine ndaŵasankha, ndi aŵa:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Awa ndi masiku anga osankhika a chikondwerero, masiku osankhika olemekeza Yehova amene uyenera kulengeza kuti akhale masiku opatulika a misonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.