Leviticus 23:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe aziweyule, pamodzi ndi buledi wa mphatso yoyamba uja, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta, pamodzi ndi anaankhosa amphongo aŵiri aja. Zimenezi ndi zopatulika zopereka kwa Chauta zokhalira ansembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi anaankhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe aweyule ana ankhosa awiriwo pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula, pamodzi ndi buledi wa tirigu woyambirira kucha. Zimenezi ndi zopereka zopatulika za Yehova zopatsidwa kwa ansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi ana a nkhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.