Leviticus 23:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pa tsiku lomwelo mulengeze, ndipo muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. Limeneli likhale lamulo lamuyaya kulikonse kumene mukakhale pa mibadwo yanu yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lomwelo mulengeze za msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.