Leviticus 23:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku lalikulu la Sabata, lopumula, tsiku la msonkhano wopatulika. Musamagwira ntchito iliyonse. Limenelo likhale tsiku la Sabata la Chauta kulikonse kumene mukakhale.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku asanu ndi limodzi azigwira nchito; koma lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira nchito konse; ndilo sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.