Leviticus 23:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Likhale ngati tsiku lalikulu la Sabata lopumula kwa inu, ndipo musale zakudya. Pa tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, kuyambira madzulo ake mpaka madzulo ena otsatira, musunge tsikulo monga ngati la Sabata.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzichepetse; tsiku lachisanu ndi chinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Limeneli kwa inu ndi tsiku la Sabata lopumula, ndipo muyenera kusala zakudya. Kuyambira madzulo a tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi mpaka madzulo ena otsatirawo muzisunga tsikulo ngati Sabata lanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzicepetse; tsiku lacisanu ndi cinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.