Leviticus 23:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku asanu ndi aŵiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Chauta. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzichita msonkhano wopatulika ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Chauta. Umenewu ndi msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zotopetsa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lachisanu ndi chitatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira ntchito ya masiku ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Kumeneku ndi kutsekera kwa msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zolemetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lacisanu ndi citatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira nchito ya masiku ena.