Leviticus 23:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ameneŵa ndi masiku achikondwerero osankhidwa olemekeza Chauta, amene muziŵalengeza kuti ndi nthaŵi ya msonkhano wopatulika. Masiku ameneŵa muzipereka kwa Chauta nsembe zapamoto, monga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zanyama, ndi zopereka za chakumwa, iliyonse pa tsiku lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lakelake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(“ ‘Amenewa ndi masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova, amene muziwalengeza kuti ndi nthawi ya msonkhano wopatulika. Masiku amenewa muzipereka nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, nsembe zanyama ndi zopereka zachakumwa za tsiku ndi tsiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lace lace;