Leviticus 23:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mutakolola dzinthu m'dziko mwanu, muchite chikondwerero cha Chauta pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku loyamba likhale tsiku lalikulu lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu likhalenso tsiku lalikulu lopumula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutatuta zipatso za m'dziko, muzisunga chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lachisanu ndi chitatu mupumule.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Choncho kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutakolola zinthu mʼmunda mwanu, muchite chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba ndi tsiku lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu ndi lopumulanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi ciwiri, mutatuta zipatso za m'dziko, muzisunga madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lacisanu ndi citatu mupumule.